M’tsogoleri wa chipani chotsutsa boma cha The Movement For Democratic Change a Morgan Tsvangirai m’dziko la Zimbabwewa dzuzula m’tsogoleri wa dzikolo president Robert Mugabe kaamba kamphekesera yoti akufuna kulanda mwa mtopola minda ina ya alimi achizungu m’dzikolo.
Malinga ndi malipoti a News 24 ati a Morgan Tsvangiraiawuza a Mugabe kuti ndibwino kuti abwere ndi njira zina zothandizira pa ntchito zokweza chuma cha dzikolo ndi kupewa kulandi minda ya alimi a achizungu.
Iwo ati ngati a Mugabe atachitenso izi ndiye kuti zithandizira kukolezera mavuto a zachuma omwe ali m’dzikomo.
Dziko la Zimbabwe ndi limodzi mwa mayiko a u Africa amene analanda minda ya azungu kamba ka nkhani za ndale.