Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Akatekist A Ku Malawi Defense Force Apuma Pa Ntchito Yawo

$
0
0

Yemwe anali Katekist  ku Malawi Defense Force a Benard Mukhula ku Zomba awayamikira kamba kodzipeleka pa ntchito yawo yotumikira mulungu kudzera mu mpingo wakatolika.

Bambo Augustine Likado ndi omwe anena izi pambuyo pa mwambo wa msembe ya misa yomwe amasanzikana ndi agulupawa Katekist Benard Mukhula ndi m’modzi mwa omwe akupuma pa ntchito yawo ku Malawi Defence Force ku Zomba.

Bambo Likado ati zomwe akatesti-wa amachita zinali zinthu zotamandika kamba koti amadzipeleka ku ntchito ya usilikali komanso ku mpingo zomwe anati zasonyeza kudzipeleka kwawo pa ntchito zotumikira mulungu kudzera mu mpingowu.

Polankhulanso a Katekist Mukhula anati ndi wosangalala kamba koti mulungu wakhala akuwasamalira komanso kuwatetedza pa ntchito yawo mu zaka zomwe akhala akutumikira mpingowu ku malowa. 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>