Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Bungwe La MHRC Lalimbikitsa Ofesi Ya Social Welfare Kuti Isachite mantha pogwira nthcito zake.

$
0
0

Bungwe la Malawi Human Rights Commission lalangiza akuluakulu omwe amaona za ma ufulu a ana ku ofesi yoona za chisamaliro cha wanthu ya Social Welfare m’boma la Zomba kuti azigwira ntchito yawo mopanda mantha.

Mkulu woona za ma ufulu a ana m’bungweli a mai Noris Mangulama Chirwandi omwe anena izi pa mkumano wa bungweli ndi akuluakulu a ku ofesiyi.

Iwo ati ofesiyi ikuyenera kumadzipeleka ndi kuonetsetsa kuti ikutetedza bwino ana , makamaka amasiye ndi ovutika amene amakhala akulandira chisamaliro kwa anthu ena akufuna kwabwino ndi m’malo ena momwe anawa amalandililamo chisamaliro chawo.

Polankhulanso registrar wa ku bwalo lalikulu la milandu laHigh Courtmu m’dzinda waZomba, mai Jean Kayira anadzudzulanso amai amene akumakonda kukatseketsa milandu yogwilira ana ndipo ati izi zikukoledzera nkhanza pakati pa ana ambiri omwe akumagwililidwa mdziko muno. 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>