Apolisi m’boma la Mchinji agwira anthu atatu omwe akuwaganizira kuti ndi mbava zoopsa kwambiri zomwe zakhala zikubera anthu m’madera osiyanasiyana m’bomalo.
Ofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Inspector Kaitano Lubrino, wati m’modzi mwa anthu-wa ndi Binali Mataka, wa zaka 35 zakubadwa anamugwira potsatira kubedwa kwa ndalama mu sitolo ya Metro m’bomalo.
Malingana ndi atolankhani a Malawi News Agency (MANA) , mkuluyi ndi amzake ena awiriwo omwe ndi a Gerald Yassin Chilumpha ndi Pemba Katinji ndi omwe akuwaganizira kuti anaba ndalama zokwana pafupifupi 3 Million, 24 Thousand Kwacha zomwe zinali mu sitoloyo.
Anthu atatuwo akaonekera ku khothi posachedwapa kuti akayankhe milandu yawo.