Bungwe la Association for Prograssive Women (APW) m’boma la Neno layamikila anthu a m’dera la mfumu Symon m’bomalo kamba kotenga nawo mbali polondoloza ntchito za zichitukuko zomwe zikuchitika m’bomalo.
Mkulu woyendetsa ntchito za bungweli a Richard Banda ndiwo ananena izi pambuyo pa mkumano omwe bungweli linakonza ndi komiti yowona zachitukuko la m’dera la mfumu yaikulu Symon m’bomalo. Malingana ndi a Banda, kudzera mu ntchito yolondoloza kayendetsedwe ka zitukuko zakuderali yotchedwa Citizen Action for Local Government (CALGA) yomwe bungweli likuyendetsa m’boma la Neno zathandiza kuzindikiritsa anthu za udindo wawo pa ntchito yolondoloza zitukukozi.
M’modzi mwa akuluakulu oyendetsa ntchito zachitukuko m’dera la mfumu yaikulu Symon a Ben Thozi-Thoza Dimba ati pakadali pano anthu am’derali akutha kudziwa kuchuluka kwa ndalama zomwe zitukuko zosiyanasiyana zikugwiritsa ntchito zomwe ati zachepetsa kuba ndalamazi ndakhalenso chinyengo. Iwo apempha kuti gwirizano umenewu upitilire ndipo kuti ufalikira m’madera ena.