Mabanja achikhristu m’dziko muno awapempha kuti adzithandiza anthu osowa ngati njira imodzi yoonetsa chifundo komanso chikondi kwa anhtuwa.
Banja la a Mapemba lomwe limapezeka ku parishi ya St Johns, Msamba ku arch-dayosizi ya Lilongwe ndilo lapereka pemphori pomwe bungwe la mabanja achikhristu ku parishi-yi limakapereka thandizo la katundu wosiyanasiyana kwa anthu ovutika omwe amakhala ku Area 36 mu m’dzinda wa Lilongwe. Banjali linapempha mabanja ena achikhristu kuti apitilize kuthandiza anthu ovutika amene ali nawo pafupi.
M’modzi mwa anthu amene analandira thandizoli ndi mayi Christina Gabriel ndipo iwo anati zomwe akhristuwa anachita zinali zamtendo wapatali ndipo zinasonyeza chikondi chopambana chomwe iwo anali nacho pa anthu ovutika.
Katundu yemwe anaperekedwa kwa anthuwa anali monga soya, ufa, ndi zina zambiri.