Chiwerengero cha anthu odwala matenda a Fistula chikukwera kwambiri kuchigawo chaku m’mawa kwa dziko lino.
Mkulu woona zamatenda a Fistula pachipatala cha boma la Mangochi a Ramzy Zinganindi omwe anena izi pofotokonzera atolankhani a Malawi News Agency MANA. A Zingani ati kukhala opanda ukhondo komanso kutenga mimba atsikana ali achichepere ndi zinthu zimene zikokolezera kukula kwa matendawa m’chigawocho.
A Zingani apempha amai komanso atsikana kuti akaona zizindikiro zakutuluka magazi kumalo awo obisika azikanena kuchipatala chomwe ali nacho pafupi mwansanga kuti azikalandira uphungu woyenera pofuna kuthana ndimavuto komanso imfa zomwe zimabwera kaamba ka matendawa.
Matenda a Fistula akukula kwambiri kuchigawo cha kum’mawa komwe kukupezeka ma boma monga a Mangochi, Machinga kungotchulapo ochepa.