M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco walonjeza kuti apereka ndalama pafupifupi 5 handred sauzande dollars ku dziko la South Sudan.
Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican, izi zadziwika dzulo lachitatu pa msonkhano wa olemba nkhani omwe unachitikila ku Vatican. Polankhula pa msonkhanowo, mkulu mu ofesi yowona za chitukuko cha anthu ku ofesi ya a Papa Cardinal Peter Turkson wati ndalama zomwe zaperekedwa ku dziko la South Sudan zigwiritsidwa ntchito potukula ntchito za maphunziro, umoyo komanso ulimi m’dzikomo.
Cardinal Turkson wati ndalama zimenezi ziperekedwa kudzera m’mabungwe a mpingo wakatolika omwe akugwira ntchito zawo m’dzikomo. Pa msonkhano omwewo, Cardinal Turkson anati Papa Francisco wapempha anthu a m’dziko la South Sudan kuti aleke kumenyana komwe kukuchitika mdzikomo. Kumenyanaku kunayamba chaka cha 2013.