Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Ma Dalaivala A Minbus Anyanyala Kugwira Ntchito Yawo

$
0
0

Madalaivala a ma Minbus ku Zomba ayamba ayima kugwila ntchito potsatila kukhadzikitsidwa kwa lamulo latsopano loti asamanyamule matumba olemera 50 kilogalamu komanso kuti asamatenge anthu anayi pa (4) pa mpando.

M’modzi mwa madalaivala-wa a Andrew Tayimu wauza Radio Maria Malawi kuti malamulo aikidwa-wa ndi omuvuta kaamba koti anthu ambiri amakwera ma Minbus atanyamula katundu osiyanasiyana.

A TAYIMU ati kunyamula anhu mopyola muyeso ndikosayeneradi koma kuletsa ma Minbus kunyamula katundu ndikomwe sakugwilizana nako kaamba koti anthu omene amakwera ma Minbus-wa amakhalansomkuti anyamula katundu.

Ndipo iwo ati akanakonda kuti apolisi a pa nsewu azigwira ma MinBus okhawo omwe alibe zowayenereza kuyenda pa nsewu monga matayala okutha, opanda ma buleki okwanila komanso dalaivala akapezeka atamwa mowa azimangidwa chifukwa ati zimenezi ndi zomwe zikumakoledzera ngozi za pa nsewu.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>