Akuluakulu a chipatala chaching’ono cha Lumbadzi ayamikira akhristu a m’phakati wa Saint Michaels kuchokera ku parish ya Saint Matias ku Lumbadzi kamba kothandiza odwala apa chipatalacho.
M’modzi mwa anamwino pa chipatalachi mayi Prisca Chingwenembe ndiwo ayamikira akhristuwa pomwe apereka katundu wosiyanasiyana kwa odwala pa chipatalacho. Mayi Chingwenembe ati chipatalachi chikukumana ndi mavuto osiyanasiyana ndipo apempha anthu akufuna kwa bwino kuti apitirize kuthandiza odwala pa chipatalachi.
Poyankhulapo, wapampando wa m’phakatiwu a Abert Zakaliya ati m’phakati wawo unaganiza zokayendera odwalawa ndi cholinga chofuna kuwapatsa katundu woti awathandiza pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku komanso kuti adzikhala ndi chimwemwe. Iwo apempha akhristu ena kuti adzithandiza anthu ovutika ngakhale iwo ali ndi zinthu zochepa.
Katundu yemwe waperekedwa kwa odwala pa chipatalachi ndiwa ndalama zoposera 200 sauzande zomwe zachokera kwa akhristuwa.