Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Akondwela Ndi Sabata Ya Ulangizi Wa Ulimi

$
0
0

Bungwe loona za ulimi m’dzino muno la MALAWI FORUM FOR AGRICULTURAL ADIVISORY SERVICES lati ndi lokonda ndi momwe sabata ya ulangizi wa ulimi yayendera m’boma la Lilongwe.

Musabatayi bungweli linachita mkumano pakati pa alimi ndi a m’bomalo.  Wapampandawo wa bungweli Dr. Charles Masangano wati  sabatayi yathandiza kwambiri pa ntchito zokweza ntchito za ulimi m’bomalo. Iwo ati alimiwa afotokoza ena mwa mavuto omwe amakumana nawo ndipo athandizana kupeza njira zabwino zothana ndi mavutowo.

Pamkumanowu alimi ambiri okhala m’madera kumidzi anadandaula kuti alangizi ambiri akukhala m’madera a m’tauni zomwe zikupangitsa kuti alimiwa adzisowa upangili wabwino wa zaulimi.

Sabata ya ulangizi wa ulimiyi inayamba pa 19 mpaka 23 June, ndipo inabweretsa pamodzi alimi, makampani ogula ndi kugulitsa zipangizo za ulimi komanso alangizi ndi cholinga chofuna kukambilana ena mwa mavuto amene alimi a m’madera osiyanasiyana m’bomalo akukumana nawo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>