Apolisi m’dziko muno atsutsa zomwe anthu ena akunena kuti akumakolezera ziwawa zomwe zakhala zikumachitika m’dziko muno.
Mneneri wapolisi m’dziko muno a James Kadadzera ati apolisi sangalekelere anthu kuti adzikasokoneza m’miseu ndi kumawononga katundu wosiyanasiyana pamene akuchita ziwawa. A Kadadzera ati apolisi m’dziko muno akugwira ntchito yawo bwino ndipo apitiliza kutero makamaka pomagwira anthu amene amasokoneza pa nthawi ya ziwawa.
Iwo apempha anthu m’dziko muno kuti adzipeza njira zabwino zothana ndi mavuto omwe akukumana nawo m’malo momapita m’miseu ndi kumakawononga katundu wosiyanasiyana.