Boma lati liyamba kugawa chakudya posasedwapa m’maboma onse omwe akhudzidwa ndi vuto la njala m’dziko muno.
Nduna ya zofalitsa nkhani ndi kuphunzitsa anthu wolemekezeka mayi Patricia Kaliati anena izi polankhula ndi radio maria pomwe imafuna kudziwa zomwe boma likuchita pofuna kuthandiza anthu omweakhudzidwa ndivuto la njala komanso ng’amba mdziko muno.
Iwo ati chakudya chi chafika kale m’maderawa ndipo apempha mipingo kuti ithandize boma pantchitoyi.
“Tayamba kale ku Nsanje komanso ku Chikwawa komanso maboma ena ngati Balaka ndi ena. Magalimoto onyamula chakudyachi afika kale m’maderawa ndipo posachedwapa anthu ayamba kulandira.
Timadziwa kuti boma limagwira ntchito limodzi ndi boma choncho tipemphe a mipingo kuti atithandize chifukwa ife tithandiza anthu 81.6% choncho a mpingo makamaka wa katolika atithandize 18.4% ena otsalawo,” anatero mayi Kaliati.
Iwo apempha mafumu komanso adindo onse kuti awonetsetse kuti anthu ovutika omwe ali ndi vuto la njala ndi amene akupindula ndindondomekoyi.