Mkulu woona mapologalamu ku Radio Maria bambo Joseph Kimu wapempha akhristu akatolika kuti adzikhala ndi chidwi chothandiza ma choir achikatolika mdziko muno.
Bambo Joseph Kimu apereka pemphori pa mwambo wopereka mphotho kwa ma choir omwe adapambana mu mpikisano wama choir omwe Radio Maria Malawi yakhala ikuchititsa mothandizana ndi kampani ya AGMA Holdings. Bambo Kimu anathokoza banja la a Katsonga omwe ndi eni ake a kampani ya AGMA Holdings kaamba ka chidwi chawo chothandiza ma choir kudzera mu mpikisano umene-wu. Iwo anapitiliza kunena kuti akhristu akuyenera kukhala ndi udindo wothandiza ma choir awo kuti nawo athandizike pomvera nyimbo zomwe ma choir-wo amayimba ndipo analimbikitsa ma choir kuti adziyimba nyimbo zogwirizana ndi chiphunzitso cha mpingo wakatolika.
Polankhula pa mwambo-wu, a Mark Katsonga anathokoza Radio Maria kamba kopereka mwayi kwa ma choir akatolika kupikisana mu mpikisano umenewu ndipo analinjeza kuti apitiliza kuthandiza mpikisano wama choir ndi cholinga chofuna kupititsa luso la mayimbidwe mu mpingo wakatolika.