Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Adzipha Kamba Koyambana Ndi Mwamuna Wake

$
0
0

M’mayi wina wa zaka 24 zakubadwa wadzipha kaamba koti anayambana ndi mwamuna wake kwa Bvumbwem’boma la Thyolo.

Wachiwiri kwa mneneri wapolisi ku Limbe a Widson Nhlane watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati mayi-yu ndi Chrissy Danielndipo ati wadzipha kamba koyambana ndi mamuna wake. A Nhlane ati bambo wa m’nyumbamo anauza mkazi wake kuti alangize mwana wawo wamkazi yemwe khalidwe lake bamboyo samagwirizana nalo. Mkaziyo sanayilandile bwino nkhaniyo ndipo anadzipha pomwa makhwala.

Iwo ati a Chrissy Daniel atamwa makhwalawo anawatengera kuchipatala chaching’ono cha Chimaliro komwe anakafika nawo atamwalira kale. Zotsatila zakuchipatalako zinasonyeza kuti Chrissyanamwalira kamba komwa makhwalawo.

Malemuwa amachokera m’mudzi mwa Kalimbuka mfumu yaikulu Chimaliro m’boma la Thyolo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>