Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Boma la Balaka Lichita Tsiku Loganizira Mwana wa ku Africa

$
0
0

Makolo ati ali ndi udindo wolimbikitsa ufulu  wa ana powonetsetsa kuti ufulu wao wa maphunziro ndi maufulu ena akukwaniritsidwa.

Bwanamkubwa wa boma la Balaka a Rodrick Mateauma ndi omwe alankhula izi ngati mlendo wolemekezeka pa mwambo woganizira tsiku la mwana waku Africa wa m’bomali omwe ma sisteri a mpingo wakatolika a chipani cha Sacramentine anachita ndi thandizo lochokera kubungwe la Catholic Relief Services omwe unachitikira mdera la Ulongwe.

Iwo ati pofuna kupititsa patsogolo chitukuko  cha dziko lino, makolo akuyenera kukhala ndi chidwi powonetsetsa kuti ana akupita kusukulu komanso sakulowa m’banja ali achichepere.

Polankhulapo Sister Ellen Matchado a chipani cha Sacramentine omwe mkulu wa sukulu ya mkombaphala ya Saint Getrude Comensoli komwe mwambowu unachitikira ati anakonza mwambowu ndi cholinga chofuna kuti ana a m’bomali akhale ndi tsogolo labwino pa maphunziro komanso kuti makolo aziwonetsetsa kuti ana akudya zakudya zamagulu onse oyenera ndi cholinga choti akule mwathanzi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>