Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mnyamata Afa Ndi Ngozi Ya Moto

$
0
0

Mnyamata wina wafa pa ngozi ya moto wa petulo umene unabuka mu golosale yake yomwe inali pa msika wa Chisamba m’boma la Ntchisi.

Ofalitsa nkhani za apolisi m’bomali Sergeant Gladson Mbumpha watsimikdzira za nkhaniyi ndipo wati malemuyu ndi Nicholas Jonathan ndipo anali ndi zaka 19 .

Malingana ndi a M’bumpha  ati motowo unabuka kamba ka kandulo yomwe amaunikira mu golosaleyo. Thupi la malemu-yi atalitengera ku chipatala chaching’ono cha Malomo m’bomalo ndi komwe atsimikiza kuti malemuyu wamwalira kamba ka motowu.

Pakadali pano apolisi m’bomalo apempha anthu kuti apewe kusunga mafuta a petulo pofuna kupewa ngozi ngati yomwe yachitikayi m’bomalo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875