Boma lati ntchito yolimbikitsa kuthana ndi mbozi zachilendo zofanana ndi ntchembele zandonda zomwe zagwa mdziko muno ikuyenda bwino.
Dr. Godfrey Ching’oma omwe ndi mlangizi wamkulu woona za mbewu mu unduna wa zaulimi, chitukuko cha madzi ndi mthilira wati ngati alimi angatsatile bwino ndondomeko zomwe undunawu ukuwaphunzitsa kudzera kwa alangizi azaulimi m’madera omwe akukhala kungathandize kupulumutsa mbewu zawo ku mbozizo ndipo alimiwo atha kukolola zochuluka.