Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wayamikira bungwe la ma episkopi a mdziko la Poland kamba ka chisamaliro chabwino chomwe anamuwonetsera pa mwambo wa chaka cha achinyamata pa dziko lonse chomwe chimachitikira mdzikolo mwezi watha.
Kudzera mu kalata yomwe mtsogoleri wa mpingo wakatolikayu walembera bungweli, iye anali ndi chidwi kaamba ka chikhulupiliro komanso chiyembekezo cha mphamvu chomwe akhristu a mdzikolo ali nacho posatengera mavuto omwe akukumana nawo.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican mu kalatayi Papa walonjeza kuti apitiriza kulipemphelera dziko la Poland kuti lipitirire kupita patsogolo mu chikhulupiliro posatengera mavuto omwe dzikolo likukumana nawo.