M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Fransiskolamulungu anachita mapemphero a padera opemphelera anthu onse omwe akhudzidwa ndi chiwembu cha mabomba chomwe chachitika ku m’mwera kwa dziko la Turkey.
Malipoti a wailesi ya Vatican ati mapemphero-wa anachitikira pa bwalo la tchalitchi lalikulu la St. Peter’s ku Rome pomwe amapemphelera anthu makumi asanu omwe afa ndipo ena ochuluka omwe avulala pa chiwembuchi.
Pa mapemphero-wa Papa ndi akhristu omwe anasonkhana pa bwaloli anapempheleranso mtendere m’dziko la Turkey. Malinga ndi malipoti gulu la zauchifwamba la Islamic State (IS)ndi lomwe lachita chiwembuchi.