Anthu a m’boma la Mulanje awapempha kuti amange ubale wabwino ndi apolisi pofuna kuthana ndi m’chitidwe wa za umbanda ndi umbava m’bomalo.
A Isaiah Mlowoka omwe ndi mkulu wa apolisi m’bomalo alankhula izi pa Likhubula Trading Center, pomwe ofesi yawo imakumana ndi anthu a zamalonda m’bomalo. A Mlowoka alimbikitsanso anthu ochita za malonda m’bomalo kuti nawo akuyenera kukhala patsogolo pa ntchito zilimbikitsa ntchito za chitetedzo cha m’bomalo kamba koti ndi amenenso ali ndi katundu wofuna kulandira chitetedzo ndi chisamaliro chokwanira.
Polankhulapo khansala wadera la Limbuli a Emmanuel Bambala anathokoza apolisi m’bomalo kamba kofika ndi mauthenga ilimbikitsira za chitetedzo ku delaro ndipo anatsimikizira apolisiwo kuti malangizo onse omwe apelike akhale akutsatidwa.
Pa mkumanowu apolisiwa azindikilitsano anthu ochita za malonda m’bomalo kuti apewe kusunga zinthu zomwe zimakolera moto mwa m’sanga m’nyumba zawo monga mafuta a petro, diesel ndi paraffin pofuna kupewa ngozi za moto , zomwe zimakondanso kuchitikanso mmadera osiyanasiyana a m’dziko muno.