Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Awapempha Kuti Adzitumiza Ana awo ku Sukulu za Mkombaphala

$
0
0

Makolo a m’boma la Zomba awapempha kuti adzikhala ndi chidwi chotumiza ana awo osachepera zaka zisanu ku sukulu za mkomba phala.

Mmodzi mwa akuluakulu ku Estate ya Gala m’boma la Zomba mai Meria Milli ati ndi cholinga cha Estate-yi kuwonetsetsa kuti ana achichepere ozungulira derali akupita ku sukulu, choncho ndi udindo wa makolo kugwiritsa ntchito mwaiwu. Iwo ati ngati makolo aonetsa chidwi pa maphunziro a ana awo, anawo adzakhala ndi chidwi pa maphunziro awo zomwe zidzapititse pamwamba maphunziro m’dziko.

Mai Meria Milli anapereka pemphori kwa makolowa pomwe bungwe loona za ulamuliro wabwino, ufulu wa anthu ndi maphunziro mogwirizana ndi ofesi yoona za chisamaliro cha anthu ya Social Welfare m’boma la Zomba inakayendera sukulu ya nkombaphala yomwe ili pa Estateyi. 


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>