Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mpingo Ulimbikitsa Mabanja Kukhala Olimba, Okhazikika mu Chikhristu

$
0
0

Mpingo wakatolika m’dziko muno wati udzipereka polimbikitsa mabanja opezeka mu mpingo-wu kukhala olimba ndi okhazikika pa chikhristu chawo.

Mkulu wa kuofesi yoona za mabungwe a utumiki wa a Papa ku likulu la mpingowu m’dziko muno la Episcopal Conference Of Malawi (ECM), bambo Vincent Mwakhwawa anena izi pofotokozera Radio Maria Malawi pamene amafuna kudziwa zina mwa zimene nthumwi zochokera m’mayiko osiyanasiyana kuphatikizapo kuno ku Malawi zinakambilana pa msonkhano wa mabanja umene unachitika m’dziko la America ndi ku Mexico mu July chaka chino.

Bambo Mwakhwawa ati msonkhano-wu unali wopambana ndipo nthumwi zinakambirana mfundo zabwino zomwenso zithandize kwambiri pa chitukuko cha ma-a-nja mu mpingowu m’dziko muno.

“Kunali ku tsindika udindo wa mabanja ntchito yawo ndi kulalika nthenga wabwino, kulalika chikondi, kugawa chikondi pa dziko lonse lapansi. Nthawi yakwana yoti mabanja alalike nthenga wabwino mwamphamvu kuyambira eni ake mayi ndi bambo komanso ana. Choncho banja lonse lili ndi mphamvu yolalika nthenga wabwino,” anatero bambo Mwakhwawa.

Iwo apempha mabanja achikhristu kuti alowe mu bungweli ndipo ati mabanja akuyenera kumakhala moyo wachikhristu.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>