Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wati pakuyenera kukhala kukambirana kwabwino pakati pa dziko la Israel ndi Palestine potsatira zamtopola komanso kuphedwa kwa anthu a mmaikowa.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican Papa ati wakhala akutsatira zamtopola zomwe zakhala zikuchitika ku malo oyera a Yerusalemu a chipembedzo cha chisilamu ndipo wapempha anthu akufuna kwabwino kuti akhale naye mmapemphero ndi cholinga choti mbali zonse zokhudzidwa pa kunsamvanaku zigwirizane mwa mtendere.
Magulu odzetsa chitetezo a mmaiko a Israel ndi Palestine akhala akuchitirana zamtopola potsatira ndondomeko yatsopano ya chitetezo yomwe yakhazikitsidwa ku malowa.