Anthu ogwira ntchito m’boma makumi awiri ndi anayi 24 afa ndipo ena makumi anayi ndi awiri 42 avulala bus yomwe anakwera itaphulitsidwa mu mzinda wa Kabul lomwe ndi likulu la dziko la Afghanistan.
Zigawenga za Taliban ati zavomera kuti ndi zomwe zachita chiwembuchi ndipo chachitika pa nthawi imene miseu ya mu mzindawu inali yotanganidwa.
Malipoti a News 24 ati aka ndi kachiwiri chiwembuchi cha mtunduwu kuchitika mdzikolo kwa anthu ogwira ntchito m’boma pomwenso chaka chatha anthu ena ogwira ntchito mu unduna wina wa mdzikolo anaphedwa.