Akhristu a mpingo wa katolika mdziko muno awapempha kuti azikonda kulowa bungwe la awerengi chifukwa ndi bungwe lomwe limazama kwambiri pa kuwerenga mawu a Mulungu.
Wapampando wa bungwe la awerengi pa tchalitchi la St. Francis ku parish ya Chisitu mu arkidayosizi ya Blantyre a Blessings Ndenguma anena izi pamene bungwe lawo limakondwelera tsiku la nkhoswe ya bungwe lawo Augastino oyera.
ANdenguma ati mamembala awo amayamba awerenga kaye ndi kuzama nawo mawu a Mulungu asanakawerenge pa mwambo wa misa kapena pa mapemphero.
“Timazama kwambiri ndi mawu a Mulungu chifukwa timakhala tikuwerenga kukonzekera bwino mawu wa sabata yathunthu tisanakawerenge pa misa. izi zimatithandiza kumvetsa bwino mawu komanso kuti tithe kuwauza ena bwino za uthenga wa Mulungu kuti amvetse bwino,” anatero a Ndenguma.
Iwo ati bungwelinso limalimbikitsa anthu kukhala otsatira ma sakramenti a mpingo wa katolika kaamba koti sililora munthu amene ali wodulidwa ma sakramenti kulowa nawo mu bungweli.