Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mabungwe Agwiritse Ntchito Radio Maria Malawi Ngati Chida Chofalitsira Nthenga wa Mulungu

$
0
0

Bungwe la Legio Ya Maria lochokera ku Kachebere mu arkidayosizi ya Lilongwe lapempha mabungwe osiyanasiyana mu mpingo wa katolika kuti azigwiritsa ntchito Radio Maria Malawi ngati chida chofalitsira uthenga wa Mulungu.

Wampando wa bungweli, a John Dulamoyo anena izi pambuyo poyendera likulu la Radio Maria Malawi ku Mangochi.

A Dulamoyo ati pa ulendowu, apindula koposa zomwe ziwathandize kutumikira Mulungu modzipereka.

“Timakhala ndi chidwi ndi momwe wailesiyi imagwilira ntchito choncho timafuna kuti tizawone mmene wailesiyi imagwilira ntchito zake. Aliyense atha kutenga nawo mbali pamapologalamu a wailesiyi kuti nafenso tifalitse uthenga wathu ngati a legio komanso mabungwe ena onse komanso kuti anthu adziwe kuti bungwelo limachita chani mu mpingo,” anatero a Dulamoyo.

A Dulamoyo apemphanso anthu onse mdzxiko muno kuti azithandiza Radio Maria Malawi kuti ipitirize kufalitsa utheng wa Mulungu ponseponse.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>