Akhristu a mu Arch-Dayosizi ya Blantyre awapempha kuti alembetse maina awo kuti azatenge nawo mbali pa sonkhano waukulu wa mabanja omwe uzachike kuyambira pa 4 ndi kutha pa 5 August mu Arch-Dayosizi ya Lilongwe.
M’modzi mwa atsogoleri omwe akuyendetsa za msonkhanowu a Kelvin Chifunda ndiomwe anena izi poankhula ni Radio Maria Malawi pomwe komitiyi yapeza kuti akhristu ochepa a mu Arch-Dayosiziyi ndiomwe aonetsa chidwi chokakhala nawo ku msonkhanowu.
Iwo ati msonkhanowu ndi ofunika kwambiri kaamba koti maepiskopi a mpingowu mdziko muno atha kuzindikira mavuto omwe mabanja achikhristu akukumana nawo