Akhristu a mpingo wakatolika m’dziko muno awayamikira kamba kopeleka molowa manja m’miyambo yonse yomwe mpingowu umakhala ukupempha thandizo kuchokera kwa iwo.
Likulu la mpingowu ku Rome m’dziko la Italy , kudzera mwa m’tsogoleri wa mpingowu padziko lonse Papa Francisco ndi lomwe lanena izi kudzera m’chikalata chomwe latumizira mpingowu m’dziko muno , chomwe kwambiri chili ndi uthenga wothokoza akhristu a mpingowu m’dziko muno kamba kopeleka mowolowa manja mu zopeleka zawo chaka chatha.
Malingana ndi mkulu ku ofesi yoona za utumiki wa a papa m’dziko muno ya Pontifical Mission Societies (PMS) yomwe ikupezeka ku likulu la mpingowu ku Episcopal Conference of Malawi (ECM) Bambo Vincent Mwakhwawa, mpingo wakatolika m’dziko muno unapeleka ndalama zokwanira 25 million kwacha , zomwe ndi zambiri kusiyana ndi momwe mpingowu wakhala akukupelekera zaka za m’buyomu.