Mfumu Mpinganjira ya m’dera la mfumu yayikulu Mponda m’boma la Mangochi yapempha omwe alowetsa zinamwali m’bomali kuti adzatulutse mwansana zinamwalizo.
Iyo yati kutulutsa nsanga zinamwali kudzapangitsa kuti ana omwe ali ku zinamwaliwo adzakhale ndi nthawi yabwino yokonzekera kuyamba kwa telemu yawo yoyamba ya maphunziro a chaka cha 2017-2018.
Pamenepa mfumuyi yapemphanso mafumu kuti akuyenera kuonetsetsa kuti m’midzi mwawo , simukuchitika miyambo ndi zikhalidwe zina zosokoneza maphunziro a ana ndi cholinga choti ntchito za maphunziro zipitilire kuyenda bwino.
Polankhulanso m’phunzitsi wa mkulu pa sukulu ya pulayimale ya Changamire yomwe ikupezeka m’dera la mfumu yayikulu Mponda a Jackson Gumbala wati kuchita Zinamwali sikolakwika , koma sizoyenera kuti zinamwalizo zizisokoneza maphunziro a ana.