Bambo wina wa zaka 25 zakubadwa m’boma la Nkhotakota wadzipha podzimangilira atamvetsedwa kuti mkazi wake akuchita chibwenzi cha nseli ndi mwamuna wina.
Malingana ndi wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Paul Malimwe, malemu-yi Masauko Makiyi anadzipha pa 2 August kamba ka nkhani-yi.
Padakalipano apolisi ati apitiliza kufufuza mpaka atapeza zotsatira zeni zeni za imfa ya malemuyi.
Malemuyi Masauko Makiyi amachokera m’mudzi mwa Mvula m’dera la mfumu yayikulu Mphonde m’boma lomwelo la Nkhotakota.