Anthu a m’dera la Chingale m’boma la Zomba ati ndi okhutira ndi ntchito zomwe nthambi ya chitukuko ya dayosizi ya Zomba ya Zomba Diocese Research and Development (ZARDD) ikugwira m’derali pothandiza kuchepetsa njala kudzera mu ulimi wamthilira.
Mfumu yaikulu Nkula ya m’derali yanena izi pa bwalo la mfumu Masapi pa chiwonetsero cha ulimi wamthilira chomwe nthambiyi ikuchita mderali.
Mfumu Nkula ati zomwe bungweli likuchita popereka zida zochitira ulimi wa mthilira komanso ziweto kwa anthu a mderali, zithandiza kuti anthu akhale ndi chakudya chokwanira komanso odzidalira pa chuma.
“Zomwe achita a ZAARD zandisangalatsa ndipo ndikukhulupilira kuti dera langa litukuka kudzera mu ndondomekoyi,” anatero mfumu Mkula.
Wamkulu wa bungweli bambo Peter Mulomole anati makono nyengo inasintha choncho anthu akuyenera kutsata njira za makono monga ulimi wa mthilira kuti akhale ndi chakudya chokwanira.
“Boma la Machinga linakhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi chaka chatha, pano likukhudzidwa ndi chilala komanso njala. Ndiye tawona kuti ndibwino kuti tiwathandize anthu amenewa. Anthu a kuno ali ndi mwayi; madzi ali nawo pafupi mu phiri mu choncho anthu asangodalira mvula poti masiku ano nyengo inasintha. Kudzera mu ulimi wa mthilira anthu azikhala ndi chakudya chokwanira chaka chonse komanso akhala ozidalira pa chuma,” anatero bambo Mulomole.
Iwo anati bungwe la ZARDD lipitiriza kugwira ntchitoyi m’derali mpaka litafikira anthu onse omwe akhudzidwa ndi ng’amba.