Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Bomba Lapha Anthu Khumi Mdziko la Pakistan

$
0
0

Anthu khumi afa ndipo ena makumi atatu avulala potsatira bomba lomwe linaponyedwa pa bwalo lina lozengera milandu mu mzinda wa Mardan kumpoto kwa dziko la Pakistan.

Malipoti a wailesi ya BBC ati munthu yemwe wachita izi anayamba waponya bomba laling’ono asanaponye bomba lomwe laphetsa anthu mu nyumba yozengera milanduyi.

Malinga ndi malipoti, izi zachitika patadutsa sabata imodzi anthu ena anayi atakaphulitsanso dera lina la chikhristu mdzikolo.

Padakali pano palibe gulu lomwe labwera poyera kuti ndi lomwe lachita za uchifwambazi koma gulu la Taliban ndi lomwe linakaphulitsa ku dera la chikhristuli sabata yatha.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>