Ntchito yokhadzikitsa bungwe lolimbikitsa mapemphero a kolona m’maparishi osiyanasiyana akuti ikuyenda bwino mu dayosizi ya zomba.
Mkulu wa bungwe-li a Grasiano Mukunuwa ndi omwe anena izi polankhula ndi mtolankhani wathu. Iwo alankhula izi pomwe mamembala abungwe-li amalimbikitsa ntchito za bungwe-li ku magomero parish mu dayosiziyi.
Iwo ati ndi okondwa kuti ma parish ambiri apempha kale akuluakulu a bungweli kuti akakhadzikitsenso bungweli kamba koti likuthandiza kuzamitsa moyo wachikhristu pakati pa akhristu a mpingowu pokonda kupemphera kolona.
Bungwe la lokona linayambira ku parish ya Thunga mu Arch dayosizi ya Blantyre mu mwezi wa November mchaka cha 2015 ndi a Graciano Mukunuwa layamba kukhala lachikoka pakati pa akhristu ambiri a mpingo wakatolika m’dziko muno.