Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

M’nyamata Wina Ku Mangochi Atema Ndi Kupha Anthu Awiri.

$
0
0

Mnyamata wina wa zaka 25 zakubadwa ali m’manja mwa apolisi m’boma la Mangochi kamba komuganizira kuti wapha mkazi wake wakale kuphatikizaponso apongozi ake .

Apolisi ku Monkebay m’boma la Mangochi ndi omwe agwira bamboyi Stephen San yemwe ndi wa zaka 25 zakubadwa  ndipo pakadali pano amutsekulira kaamba ka mulandu wa kupha umene ndi wotsutsana ndi gawo 209 la malamulo oweluzira milandu m’dziko muno. 

M’nyamatayu akuti anali pabanja ndi mkazi amene akumuganizira kuti wamuphayu koma kuti makolo a mkaziyi anathetsa banjalo ndi kumutumizanso mwana wawo wamkaziyu kusukulu.

Pa 13 August 2017 mkazi wake wakaleyu anali pa ulendo ndi mayi ake ndipo mwadzidzi anakumana ndi mnyamatayu amene anayamba kukangana ndi mkaziyo ati ponena kuti akufuna kuti amuone mwana wake amene anabeleka naye pa nthawi imene anali kukhalira limodzi ngati banja ndipo mayi a mkazikyo ndi amene anayamba kuletsetsa nkanganowo.

Pokwiya ndi izi mnayamatayu akuti anangotulutsa chikwanje ndi kutema pakhosi pa mkaziyo ndi mayi akewo kenaka ndi kuthawa.

Anthu omwe anafika pamalowo ndi amene anapeza mkaziyo ndi mayi akewo ali magazi okhaokha ndipo atawatengera kuchitapala chaku Monkebay ndi komwe anatsimikiza kuti anthuwo anali atamwalira kamba kotaya magazi.

Malingana ndi wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo sergent Amina Tepani Daudi mnyamatayu akaonekera ku khoti ndi kukayankha mulandu wakupha.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>