Makolo omwe ana awo amaphunzira pa sukulu ya pulayimale ya St John m’boma la Mangochi awayamikira kamba kodzipeleka pa ntchito zotukula maphunziro a atsikana pa sukulu-yi.
M’phunzitsi wa mkulu pa sukulu-yi mayi Cecilia Mtambo ndi omwe anena izi potsatira ntchito imene makolo-wa agwira molumukizana ndi mafumu awo poumba ndi kuotcha njerwa, zomwe akufuna kuti amangire malo a chisamaliro cha atsikana pa sukuluyo.
Bungwe la Malawi Education Sector Implementation Project (MESIP) ndi lomwe labwera ndi ganizo lomangira atsikanawa malowa.
Polankhulanso wapampano wa bungwe lothandiza pa chilimbikitso cha atsikana pa maphunziro awo la Mother Group mayi Elizabeth Joseck anathokozanso bungweli kamba koganizira sukuluyi pa chitukukochi .