Akuluakulu a chipatala cha Thondwe m’boma la Zomba ayamikira bungwe la achinyamata la Mwana Wa M’mudzi chifukwa chomanga malo asikelo ya ana pa chipatalacho.
Mkulu wa alangizi a za umoyo ku Thondwe a Martine Muhalapa ndi omwe anena izi pomwe amayamikira ntchito yotamandika yomwe achinyamatawa agwira pomanga malowo ponena kuti izi zithandiza kupititsa patsogolo ntchito za umoyo pa chipatalapo.
Polankhulanso wapampando wa bungwe la achinyamatawa a Doreen Kalema ati malowo awamanga ndi thandizo la ndalama zomwe akhala akutolera kuchokera kwa anthu akufuna kwabwino ndipo apitiliza kulimbikira pa ntchito za umoyo ndi zina zothandiza pa chitukuko cha m’delaro