Msonkhano wa bungwe la amayi achikatolika mu dayosizi ya Mangochi wa chaka chino unayamba pa 17 August ndikutha pa 20 august 2017.
Amayi ochokera m’ma dinale onse opezeka mu dayosiziyi ndi omwe atenga nawo mbari pa msonkhanowu chaka chino.
Polankhula pa mwambo wotsekulira msonkhanowu bambo Frank Chingale omwe anayimira a episikopi a dayosiziyi anati amayi a mpingo wakatolika mu dayosiziyi akuyenera kudziwa kuti pomwe akugwira ntchito zotumikira mulungu azikhala akukomana ndi zina zowapinga pa utumiki-wu koma sakuyera kugonjera izi koma kukhala olimbika odzipereka pa chikhristu chawo.
Mlendo wolemekezeka ku mwambowu anali mayi Lilian Patel omwe ndi phungu wa kunyumba ya malamulo woyimira dera la ku mwera kwa boma la Mangochi.
Iwo analimbikitsa amayiwa kuti akhale okondana chifukwa akalimbikitsa izi ntchito za bungwe lawo zidzapita patsogolo.
Malingana ndi wapampando wa bungweli mayi Mary Maganga anati zina mwa zimene amayiwa azigunda kuti akambilane mkatikati mwa msonkhanowu ndi monga za mchitidwe wozembetsa anthu human trafficking ndi zina zothandiza pa chitukuko cha mpingo ndi miyoyo yawo.