Ntchito yopeleka luso losiyanasiyana pakati pa amayi mu mpingo wakatolika mu arch-dayosizi ya Lilongwe akuti ikukomana ndi mavuto osiyanasiyana.
Bambo Francis Lekaleka , omwe ndi bambo mlangizi wa amayi mu dayosiziyi , ndi omwe anena izi polankhula ndi radio maria malawi.
Iwo ati kusowa kwa zipangizo ndi kusowa chidwi kwa amayi ena , ndi ena mwa mavuto omwe akusokoneza mapulani antchito-yi mu arch-dayosizi-yo.