Mpingo wakatolika m‘dziko muno wapempha achinyamata kuti azikhala omasuka pofotokozera mpingo, pa zamavuto omwe amakhala akukomana nawo.
Mlembi wa mkulu , ku likulu , la mpingo wakatolika mdziko muno, ku Episicopal Comference Of Malawi (ECM) , bambo Henery Saindi, ndi omwe anena izi pakutha pa msonkhano wa achinyamata ndi nthumwi zochokera ku bungwe la Amecea umene umachitikira mu mdzinda wa Lilongwe ndipo m’mawu awo ati achinyamata akuyenera kukhala omasuka makamaka pa nkhani zokhuzana ndichipembedzo kuti azikhala ndi moyo wamphamvu pa chikhristu chawo.