Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Alimbikitsa Akhristu Kulandira Masacramenti

$
0
0

Akhristu a mpingo wakatolika m’dziko muno awalimbikitsa kuti azikonda kulemekeza Sacrament la Ukaristia kamba koti sacramentili ndi limodzi mwa ma sacrament opamba pakati pa akhristu mu mpingowu.

Bambo Edwin Lambulira , omwe amatumikira mu Parish ya Kausi mu dayosi ya Mangochi , ndi omwe anena izi pomwe amatsogolera mwambo wopeleka sacramentili koyamba kwa akhristu ena ampingo-wu.  

Bambo Lambulira alangiza akhristu omwe ayamba kulandira sacramenti-li mu parishi-yi kuti adzikonda  kumadziyeletsa polapa zakwayipa zawo , ndi kuti pomwe akulandira sacramenti-li adzikhala ali anthu oyera mitima, zomwenso zimathandiza kumanga ubale wabwino ndi mulungu.

Mwambo-wu unachitikira ku tchalichi la St John yomwe ndi nthambi ya parish ya Kausi mu dayosiziyi.               


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>