Episkopi wa dayosizi ya mpingo wakatolika ya Mangochi Ambuye Montfort Stima apempha akhristu a mpingo wakatolika m’dziko muno kuti chaka cha jubilee ya chifundo cha Mulungu chisanathe apite ku malo oyera aliwonse amene akupezeka m’dziko muno kuti akapemphere ndi kulandira chifundo cha Mulungu.
Ambuye Stima alankhula izi pa mwambo wa mapemphero a chifundo cha Mulungu komanso wodalitsa guwa lomwe lamangidwa ku phiri loyera la Unangu lomwe likupezeka mu dinale ya Mpiri mu dayosizi ya Mangochi.
Iwo ati kupatula kupita kutchalitchi lamulungu lililonse, akhristu amayeneranso kuchita ntchito zauzimu komanso kupereka mapemphero apadera monga kupita ku malo oyera ndi kukatula nkhawa zawo.
“Papa Francisco akutipempha kuti mchaka ichi cha chifundo tichite ntchito zachifundo komanso tiyendere malo oyera kukapemphera ndi kupempha chifundo cha Mulungu. Choncho ife lero tinali kuno kupemphera komanso kudzadalitsa guwa limeneli lomwe kuyambira lero pazichitikira miyambo yoyera yosiyanasiyana. Ndikupempha akhristu onse omwe chiyambireni chaka cha chifundochi sanapite ku malo oyera kukapemphera kuti masiku atsalawa ayesetse ndithu apite ku malo oyera ndi kukayanjana ndi Mulungu,” anatero Ambuye Stima.
Ambuye Stima ati anthu asamangoganiza kuti malo oyera ndi maiko a kunja okha koma ati mdziko muno malo oyera aliponso omwe anthu akapemphera amalandira chifundo cha Mulungu.
Polankhulanso pa mwambowu wamkulu wa dinale ya Mpiri komwe kukupezeka malo oyerawa Bambo Medrick Chimbwanya ati malowa ndi othandiza kwa akhristu onse mdziko muno ndipo anati mapemphero awo atsikuli ndi chisonyezo cha umodzi pakati pa akhristu a mu dinaleyi, Papa Francisco komanso mpingo wonse wa Eklezia katolika mu chaka ichi cha chifundo.
“Dinale yathu inakonza mapemphero amenewa ngati njira imodzi yolumikizana ndi Papa Francisco mu chaka ichi cha chifundo kuti kupatula kuchita ntchito za chifundo tikuyeneranso kuyenda kukapemphera ku malo oyera. Poyamba tinalibe guwa kumalo kuno ndiye miyambo yake timachitira malo osalongosoka koma kuyambira lero tili okondwa kuti tizichita miyambo yathu pa guwa labwino komanso lodalitsidwa,” anatero bambo Chimbwanya.
Episkopi wopuma wa dayosizi ya Mangochi Ambuye Allesandro Pagani, mu kalata yawo ya m’chaka cha 2012 analengeza kuti mudayosizi ya mangochi muli malo anayi omwe ndi oyera omwe anthu atha kukapemphera ndi kulandira chifundo cha Mulungu ndipo malowa ndi monga parishi ya Utale 1, Nankhwali parish, St. Augustine Mangochi cathedral kuphatikizapo phiri la Unangu.