Msonkhano waukulu wokonzekera tsiku la nkhoswe ya dayosizi ya Mangochi akuti udzachitika loweluka likudzali pa 26 August 2017 ku likulu la dayosizi-yi ku Mangochi.
Akulikulu la dayosizi-yi ndi omwe akonza msonkhano-wu pofuna kudzakambilana mfundo zikuluzikulu zomwe zidzathandize kuti mwambo-wu chaka chino udzakhale wopambana.
Pofotokozera Radio Maria Malawi mkulu wa ku ofesi ya zofalitsa nkhani ndi mauthenga osiyanasiyana mu dayosiziyo bambo Emmanuel Malipa ati mwambo woganizira tsiku la nkhoswe ya dayosizi-yi poyamba unakonzedwa kuti udzachitike pa 26 August 2017 koma awusintha ndipo m’malo mwake udzachitika pa 7th October 2017 ku St Augastin Parish , ku Mangochi Cathedral.