Gulu la anthu a ndale la Trasformation Alliance lati tsopano lapeza malo atsopano ochitilako m’sonkhano wake waukulu.
Ofalitsa nkhani za guluri a Leonard Chimbaka wati guluri tsopano lapeza malo mu holo ya mpingo wakatolika ya Saint Pius Catholic Parish mu m’dzinda wa Blantyre komwe lidzachitireko msonkhano wake waukulu.
Msonkhano-wu awukonza kuti udzachitike kuyambira pa 25 August 2017 , ndipo udzapitilira pa 26 August 2017 ku Grace Bandawe mu m’dzinda womwe-wu wa Blantyre.
Msonkhanowu akuti unayenera kuchitikira ku College Of Medicines koma kuti guluri alikaniza kuti likachitire msonkhano wake ku malowa.