Apolisi m’boma la Machinga ati akufunafuna anthu ena omwe sakudziwika omwe afukula manda m’mudzi mwa Chinguwo kwa Sub TA Mchiguza m’bomali.
Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomali Constable DavieSulumba wati a Patson Nsabwe auza apolisi m’bomali kuti pa 18 mwezi uno, pamene amapita kuti akazonde manda a mdzukulu wawo Gayesi Sitande yemwe anaikidwa pa 16 mwezi uno monga mwa chikhalidwe, ndi mmene anapeza manda a mdzukulu wawoyu atafukulidwa.
Constable Sulumba wati akuluakulu a m’mudziwu mothandizana ndi apolisi ya Nayuchi anafukula mandawo ndipo anapeza thupi lamalemuyi lili bwinobwino koma mbali ina ya nsalu yomwe anakulungira malemuyi yotchedwa ‘sanda’ ita itadulidwa ndipo ati anapezanso lezala lili pomwepo. Padakali pano apolisi ati akuchita kaukufuku wao kuti amange aliyense amene apezeke wokhudzidwa ndi mlanduwu.