Achinyamata a m’dera la ku m’mwera cha kumadzuro kwa boma la Dowa awalimbikitsa kuti akhale olimbika pa nkhani za maphunziro.
Senior Group Village Headman Kawiri ya mbomalo ndi amene yapeleka malangizowa pomwe imapeleka ndalama ku matimu amene achita bwino pa mpikitsano wa masewero a mpira wamiyendo umene mfumu-yi inakhadzikitsa pakati pa achinyamata a m’delaro.
Mpikitsanowu unali wa ndalama zokwanira k150, 000.00 (hundred and 50 Thousand Kwacha).
Iyo inati achinyamata akuyenera kulimbikira maphunziro ndi cholinga choti dela lake lidzakhale lochita bwino pa nkhani zachitukuko.
Mwambo-wu unachitikira pa bwalo la sukulu ya pulayimale ya Kafumphi m’bomalo.