Mpingo wa Anglican wayamikira m’gwilizano wa mphamvu umene ulipo pakati a mpingowu ndi mpingo wakatolika m’dziko muno.
Mkulu wa mpingo-wu m’dziko muno Ambuye Brighton Vitta Malasa , omwenso ndi a episikopi a mpingo-wu mu dayosizi ya Uppershire ndi omwe anena izi polankhula ndi mtolankhani wathu.
Iwo ati mpingo wa Anglican upitiliza kulimbikitsa umodzi umene ulipo pakati pa mipingo-yi ndipo apempha akhristu a mipingo iwiriyi kuti azigwilira ntchito zawo limodzi pofuna kupititsa patsogolo umodziwu.