Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Azipha pozimangilira mboma la Mangochi.

$
0
0

Bambo wina wa zaka 60 wa dzipha podzimangilira m’boma la Mangochi.

Malingana ndi wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo sergent Amina Tepani Daudi wati bambo-yu Umali Sabiti  mutu wake unayamba kusagwira bwino ntchito  atangochitidwa za upandu ndi zigawenga za m’gulu lina ali m’dziko la South Africa. 

Iye wati chibweleleni mdziko muno akuti wakhala akulengeza kwa abale ake kuti azipha zomwe zinayamba kuchititsa mantha pakati pa achibale a bamboyu .

Ndipo masabata apitawa akuti bamboyu anasowa pakhomopo ndipo  anakapezeka pa malo ena koma atazimangilira.

Wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za apolisi m’boma la Mangochi , Seargent Amina Tepani Daudi wati malemuyi Umali Sabiti anali ochokera m’mudzi mwa Nkasanjira m’dera la mfumu yayikulu Katuli m’boma la Mangochi.  


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>