Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Apolisi Alanda Galimoto Lomwe Akuliganizira Kuti Linachita Kubedwa

$
0
0

Apolisi m’boma la Machinga alanda galimoto ina ya mtundu wa Toyota Fortuner D4D , kamba koyiganizira kuti inachita kubedwa.

Ofalitsa nkhani za apolisi m’chigawo cha ku m’mawa kwa dziko lino Inspector Joseph Sauka wati galimoto-li aligwilira mu msewu wa Bakili Muluzu High Way , ndipo imachokera mu msewu wa ntaja kupita ku Liwonde.

Amene amayendetsa galimotoli lomwe ndi nambala yake ndi RU 8817 a Davie Mkwalala alinso m’manja mwa apolisi kuti afotokoze bwino umwini wa galimotoyo. 

Malingana ndi a Sauka  galimotoli lili m’manja mwa apolisi kamba,  Koti makalata ake sakugwilizana ndi mtundu wa galimitolo.

Iwo ati zomwe apeza mukufufuza kwawo ndi zoti nambala plate ya galimotoyo ikusonyeza kuti ndi ya galimoto la mtundu wa Toyota Pick Up osati Toyota Fortuner D4D monga zinakhalira pa galimotoli.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>