Bwana mkubwa wa boma la nsanje a Gift Rappozo wati awonetsetsa kuti ndalama za mthumba la zachitukuko ku madera a aphungu m’bomalo (constituency fund) zikupinduliladi anthu okhala m’madera-wa pa nkhani zachitukuko.
A Rapozzo anena izi m’bomalo pa msonkhano wa ukulu wa makhansala (Full Council Meeting) .
A Rapozzo ati mwa zina pofuna kutetedza ndalama za m’thumbali adzionetsetsa kuti ndalama zomwe zikutengedwa mthumbali zavomelezedwanso ndi makhansala osati aphungu okha.